This webpage accompanies work to present A. E. Dziko's 'Bwampini' (1965, rev. 1975) at the Fourth International Classical Conference in Ghana, which takes place from 3rd to 4th September 2026 at the University of Ghana, Legon, Accra.
It collects transcripts of the two original texts (1965 and 1975), in Chinyanja / Chichewa, together with recordings, a translation of the 1975 text into English (the first), indices, dramatisation of one of the chapters and a certain amount of other material. It is intended to expand this collection in due course.
Text
1975
[01.01]
Kudali msonkhano wa dziko lakumwamba, Kuntheradi kumene anthu anzeru zapamwamba anali kukhala. Iwowo kwenikweni sanali anthu, ngakhale adali ndi matupi chifukwa chanzeru zawo zakuya.
[01.02]
Anthuwa dzina lawo lidali Azimu. Msonkhanawo adauchititsa ndi mfumu ya Azimu onse dzina lake Tinjiwa. Iyeyu adali ndi mkazi wake dzina lake Ngapagwa. Adali ndi abale ake awiri, Chimphanza ndi Ndomondo, amenewa kwenikweni adali aphwake.
[01.03]
Tinjiwa adabereka ana ake ambiri. Wachisamba adali Mbamba, mnyamata wochenjera ndiponso wokonda za chipala. Wachiwiri adali wamkazi, dzina lake Mziisi. Ngakhale adali wamkazi, iyeyu adali wamphamvu kwambiri. Mphamvu zake zidaposa mwamuna aliyense.
[01.04]
Wachitatu adali mnyamata wokongola kwambiri dzina lake Mapiko. Iyeyu adali ndi thupi lopepuka. Pa zothamanga zokha adalibe mnzake. Popeza azimu [Azimu] onse adali wotha kuuluka chibadwire, iyenso ankauluka kwambiri moti njiwa siikadapikisana naye.
[01.05]
Mapiko adapondana ndi Chang’aning’ani [Ching’aning’ani], mtsikana wokongola koyiwalitsa zambiri. Pambuyo pa ameneyu padabadwa chim’nyamata chomvetsa kaso, dzina lake Chezichezi. Luso loyimba ndi lopanga zosema lidalidi lakelake. Chezichezi adali wodziwa kuyankhula ndi kuchita zanzeru ngati atate ake.
[01.06]
Azimu ena ankakwatira koma ena ankangokhala wosakwatira. Koma chifukwa chosachulukitsa pa mtundu wawo, ankakwatirana pachibale. Kotero Mbamba adakwatira mlongo wake, Ching’aning’ani.
[01.07]
Chimphanza adakwatira mdzukulu wake, Mphukeyi, mwana wotsiriza wamkulu wake. Ndomondo ali ine ndikwatira mdzukulu wangayu, chitsirizira chenicheni cha Ngapagwa. Mkazi wakeyo adali Saisi. Pa zokwatira zokha, Azimu sadasiyane ndi anthu okhala padziko la pansi.
[01.08]
Tinjiwa poona kuti dziko lili kum’kulira, abale ake ndi ana ake omwe akhwima nthenga, adaitanitsa chimsonkhano cha Azimu onse.
[01.09]
Onsewa atasonkhana m’chinyumba chochezera, iye adadzuka pa chimpando chaulemu. Nthawi yomweyo onse adakhala chete.
[01.10]
‘Mkazi wanga wamphete, aphwanga ndi ana anga onse, kusonkhana kwanu kwandikondweretsa ine, mfumu yanu. Ndati ndikuuzeni chinsinsi cha bambo wanga chimene ndachisunga ngati phukusi la mbewu. Mukulidziwa dziko lino mukukhalali. Tayang’anani pansipo. Dziko ilo likuonekalo mukulidziwa? Nanga pansi pa dziko limene likuonekalo, mukulidziwanso?
[01.11]
‘Bambo wanga adalenga maiko atatuwa: loyamba ndi lino tikukhalali; lachiwiri adalipatsa kwa anthu a pansi, mukuwaonawo; lachitatu, lili pansi penipeni, ndiye kumene ndimatumiza anthu akufa. Ife sitifa, koma apansi okhawo. Dziko lino ndi Ntheradi, la anthu amoyo ali pansiwa ndi Sachokeka, ndipo la akufawo ndi Midima. Monga mukudziwa, chintchito changachi ndi cholemetsadi. Ndimalamula maiko atatu onsewa, ndikupereka zonse zofunika. Lero mwakula aphwanga ndi ana anga ndiye ndati ndikugawireniko udindo wangawu.’
[01.12]
Chimphanza:
Akulu, ndikudulani, si chipongwe ayi, mwachita bwino kwambiri.
Onse:
Pwa! pwa! pwa! (m’manja)
Tinjiwa:
Zikomo kwambiri, tsonotu tione wotha kulamula ku Sachokeka, nyanja zonse ndi mitunda yomwe.
Mziisi:
Bambo akulu a Ndomondo, angayesere.
Ngapagwa:
Siingawalake ntchito imeneyi, ndiponso ndikuona ngati amalikonda dzikolo makamaka nyanja zake.
Onse:
Ha! ha! ha! ha! ha!
Tinjiwa:
Mukuti bwanji akulu?
Ndomondo:
Ndikamanga nyumba yanga yaufumu mu nyanja ya mchere [Nyanja ya Mchere], kum’mawa kwa dziko la anthu akuda.
Onse:
Pwa! pwa! pwa! (m’manja)
Tinjiwa:
Nanga ku dziko la anthu akufa?
Ching’aning’ani:
Bwanji kupite bambo wamng’ono popeza amakonda kumva chisoni makamaka akamwalira munthu ku Sachokeka.
Mphukei:
Kodi? Nkwabwino amunanga?
Tinjiwa:
Monga mwavomera achimwene?
Chimphanza:
Izo ndizo ndimakonda.
[01.13]
Mfumu idapitiriza kuyankhula, kuti pankasoweka mtumiki woyamba wa mithenga. Onse adamvana kuti akhale Mapiko, chifukwa ndiye adali wandawala. Kenaka adasankha ogawira luso ndi nzeru anthu a ku Sachokeka. Apo sadatsutsane kwambiri, Chezichezi adalandira ntchitoyo. Pamene adafika pa mutu wa nkhondo ndiye padali mgwegwe. Mfumu itafunsa, amene adayankha ndi Mapiko.
[01.14]
Mapiko:
Ntchitoyi ndi yoyenera munthu wamwamuna, akazi ayi. Bwanji atayesa a Mbamba?
Ndomondo:
Ntchitoyidi ndi ya munthu wamwamuna, koma mukaona amunafe timatupi tathu ndiye ngati tiziwala. Atayesa a chemwaliwa, a Mziisi, Tawaonani pamene ayimapa.
Ngapagwa:
Apodi ndi zoona sikukondera, koma Mziisi akadayesera.
Mbamba:
Tisalimbane kwambiri bambo. Ngakhale ali wamkazi, Mziisi atha kuyesera.
[01.15]
Pamenepa onse adagwirizana, Mziisi adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa nkhondo. Mbamba adasankhidwa kuti akhale mwini zida ndi chipala. Utatha msonkhano, Ndomondo ndi Saisi, mkazi wake, adauyamba ulendo wa ku Sachokeka. Nayenso Chimphanza adapita ku Midima ndi mkazi wake.
[01.16]
Tinjiwa adakondwa ndikulamula kuti chakudya cha Azimu chibwere. Azimu amadya uchi ndi chingwa, ndi kumwa manyuchi basi. Mbamba ndi Ching’aning’ani adamenyetsa zitsulo zawo m’chipala. Anthu a ku Sachokeka ndi Midima adadodoma ndipo adagwira pakamwa osamvetsa zochitika ku Ntheradi pa kumva mabingu.
[02.01]
Ku Sachokeka, dziko lachiwiri, kudali bata. Kudali mitundu yambiri ya anthu. Angitau ndiwo udali mtundu waukulu wa anthu onse. Dziko lawo lidali pafupi ndi mtsinje wa Nile ndipo linkatchedwa Ngitau. Mfumu yawo idali Zimeze, munthu watsitsi lakuda, wachinyamata, wokhuthala bwino, wamfupi, wansangala kwambiri ndiponso wokongola mwachiufumu.
[02.02]
Nachimasomaso, mkazi wake, adalidi munthu wamayi. Iye adali wachifupikire, wonenepa, tsitsi lotuwira, timaso towala, nkhope yosalala ndi yowala ndipo zonse mwa iye zidalidi m’malo mwake. Mwa akazi onse a ku Sachokeka panalibe wokongola.
[02.03]
Tsiku lina akucheza ndi mkazi wake, bwenzi lake, ndi nduna ndi mamulumuzana ake mkhonde mwa nyumba yake yokongola yachifumu, adadodoma pomva chimkokomo cha mphepo. Anthu onse adaleka kuyankhula ndi kumayang’anitsitsana. Chimphepocho tsono chidangozungulira nyumba yake.
[02.04]
Mwadzidzidzi adangoona mtambo woyera pafupi ndi nyumba yake. Onse pakhondepo poona mnyamata wamtali, wachilendo, wokongola akuchokera mumtambo, adalenguka ndi mantha ndi kugwa pansi.
[02.05]
‘Dzukani musaope.’ Liwu lomveka bwino lidatero. Onse adadzuka ndikukhala tcheru. ‘Ndine Mapiko wamthenga. Ndachoka ku Ntheradi, kumene kumakhala Tinjiwa, Mfumu ya mafumu kuti ndidzalalike ndi kupereka uthenga wake. Iye wati, kuyambira dzulo maufumu atatu agawidwa, mukuwadziwa kale maufumuwa. Dziko lakumwamba, Ntheradi; mfumu yake ndi Tinjiwa. Ufumu wa pansi pano, kuno ku Sachokeka, uli m’manja mwa Ndomondo, mkulu wake. Dziko lapansi penipeni, ku Midima, Chimphanza ndiye azilamulira.’
[02.06]
‘Uthenga wina ndi woti mukafuna nzeru muzipepempha kwa Chezichezi. Mukafuna zida za nkhondo, muzipempha kwa Mbamba, ndipo ngati ndi koyenera adzakupangirani. Mziisi ndiye wodziwa dongosolo lonse la nkhondo.’
[02.07]
Atayankhula choncho, mtambo ujanso udam’phimba. Mfumu idayang’anitsitsa nduna zake ndikufunsa kuti uthenga wa kumwamba aumvetsa bwanji.
[02.08]
‘Tichitenji?’ mfumu idafunsa. Mwa anthu onse omwe adabadwa, nayamwa mawere a munthu wamkazi nalembedwa kuti adzafa tsiku lina, sipanaoneke munthu wochenjera poyankhula ndi kuweruza milandu: ndipo padalibe wodziwa kulewa ndale za anthu, amene akadayankha chifunso chokhwima cha mfumu, koma Bwampini yekha.
[02.09]
Iyeyu adali mmodzi mwa nduna zowerengedwa za mfumu. Kwawo kudali ku Buwa dziko lomwelo la Angitau, koma kafuko kena. Pomva funso loterelo nduna zina zitatu zidaganiza zochitira chipongwe Azimu, chifukwa ankafuna kuwalanda ufumu. Ena adati, tingokhala, tione mmene ziyendere.
[02.10]
Bwampini yekha adatsutsa nati kwa mfumu ndi kwa makosana onse, ‘Poyamba ife ndife anthu, a ku Ntheradi ndi Azimu. Ife nzeru zathu zicheperatu poyerekeza ndi zawo. Sitingachite chipongwe, chifukwa mmene tikuyankhulamu akutimva. Mmene agawana maufumu chonchomu ndi bwino, chifukwa ifenso phindu lathu ndi lalikulu. Ndi nzeru zawozo adzatithandiza. Tingochita chaka posonkhanitsa anthu onse kuti amvetsetse. Tikatero tidzakondweretsa Tinjiwa poti watitumizira Ndomondo, kuti adzakhale wotiweruza pa zinthu zimene sitimvetsa ndi nzeru zathu za umunthu.’
[02.11]
Pomva mawu anzeru oterowo, mfumu, mkazi wake, nduna ndi makosana onse, adamuombera m’manja ndi kumuweramira. Mawu ake adali anzeru. Mfumu adauza nduna yake yaikulu kuti isonkhanitse anthu ake kuti akonzekere za chaka. Bwampini atafotokozera chigulu cha anthucho, monga mfumu adapempha, anthu adabalalika. Mmawa mwake, anthu adapha zifuyo monga: nkhuku, nkhosa, mbuzi, ng’ombe ndi nkhumba. Adaphika zakudya zochuluka ndi kukonza zakumwa zoledzeretsa. Anthu onse atasonkhana, mkulu wansembe, Chipempherere, adapereka nsembe kwa Azimu onse naperekanso ina yapadera yolandira ndi kuvomereza chitetezo cha Ndomondo. Ndipo anthu adadya, navina ndi kumwa kwa ndazioneranji!
[03.01]
Anthu amafanana pa kapangidwe, koma kusiyana kwawo pa zambiri ndi kwakukulu. Kudali mtundu wanzeru, waluntha ndi luso m’dziko lomwelo la Angitau dzina lake Abuwa. Iwo anali kukhala chakum’mwera m’dziko la mfumu Zimeze. Mfumu yawo idali Bwampini.
[03.02]
Bwampini adali ndi msinkhu wautali, wokulupala, wa tsitsi lobiriwira, nkhope yake idali yaifupi, phuno yake yaitali ndipo kunsonga kwake idali ngati mlomo wa chiombankhanga. Adalidi wokongola m’maonekedwe.
[03.03]
Akuluakulu amtundu waChibuwa ankati Bwampini akadali mnyamata, atsikana ankangomulondalonda, nkhalamba ndi tchembere zomwe zidamfunsirafunsira. Chachikulu kopambana, iye adapambana anthu anzake onse pa nzeru. Anthu ambiri poganiza ankati, pang’onong’ono bwenzi atakhala mwana wa Tinjiwa. Poyankhula zanzeru kapena mtsutso ndi anzake, pogamula milandu, pa masewera a mitundu yonse, padalibe mnzake.
[03.04]
Chifukwa cha zonzesi, Zimeze sadapeneke kumusankha iyeyu kukhala mulumuzana wamkulu mwa onse ndiponso nduna yake. Mwa chiganizo cha anthu ndi Azimu okhala ku Ntheradi, iye adachita mwayi wokhala ndi mkazi wolingana naye pafupifupi zonse. Dzina lake adali Namasinkho. Munthu ukakhala wanzeru, tsoka ilo mwina umakwatira chidzete, kukhala wotsetekeka, mkazako mwina amakhala kaphulika; Khungu!
[03.05]
Phula lotereli Bwampini adalibe. Adagwiradi pakatikati. Awiriwa adakondonadi; chikondi cha bulangeti! Mtendere udali wathunthu pakati pawo. Anthu odzawayendera sadaleke kuzizwa ndi udongo, ufulu ndi kumvana kotereko.
[04.01]
Ku Ntheradi kudali chimwemwe cha malipenga; nako ku Sachokeka kudali ufulu wokhawokha. Zimeze ndi anthu ake sadaleke kuthokoza Ndomondo chifukwa zonse zidayenda mwakaso.
[04.02]
Ngakhale kudali chimwemwe chotere, m’dera lina, kumene kudali anthu amtundu wina, nawonso anthu aluso (koma pang’ono), sadali osangalala kwenikweni. Kwenikweniso mtunduwu udali wopanda nsangala wofuna kutsutsulatsutsula ena pachilonda.
[04.03]
Mtunduwu unkatchedwa Agangire. Mfumu yawo idali Gangire amene. Mfumuyi idali yokalamba koma yanzeru. Munthutu akakalamba nthawi zina amatayirira pa zinthu zina. Ana ake ndiye ankangokhala ngati alowa kale ufumu.
[04.04]
Gangire adali ndi ana ake aamuna awiri, Litsipa ndi Utwa. Woyamba ndiye adali wamkulupo. Iyeyo ankakonda kumuwetetsa ng’ombe ndi zifuyo zina. Wang’onoyo, Utwa, popeza kuti adali ngati chitsirizira, ankakhala kumudzi kusangalatsa ukalamba wa atate ake. Komatu adali ndi mphamvu zambiri.
[04.05]
Tsiku lina Litsipa atapita ku ubusa, iye mbuzi zake adangozisiya pa msipu wambiri. Iye adafuna mthunzi pena, nakhala pansi. Akudzikhalira choncho akuganiza zake, chinthu china chidamudabwitsa; kudalibe mitambo konse, koma mwadzidzidzi, padaoneka mitambo itatu yoyera, chakum’mawa, youluka ndi liwiro. Posakhalitsa adayionera chapafupi. Kenaka adangoona kuti ndi anthu, atatu aimirira pafupi naye: anthu ovala zonyezimira ngati dzuwa, nkhope ngati makanda, okongola kosasimbika.
[04.06]
Iye mwaulemu adawalonjera, natonthola ndikuwayang’anitsitsa mosachita mantha. Iye adamvetsa kuti adali Azimu. Mosataya nthawi, Ching’aning’ani mkazi wa Mbamba adayankhula.
[04.07]
Ching’aning’ani:
Kodi ukudabwa? Ife tadza kudzakuchezetsa, kwina takukonda ndipo tabwera ndi mphatso. Utchule ndani mwa ife ali wokongola. Ameneyo ndiyemwe ati akupatse mphatsoyo.
Mziisi:
Komatu pamenepa uyunera kuganiza bwino. Ukatchula ine ndikupatsa mphamvu zopambana aliyense amene amamwa madzi.
Chezichezi:
Ine ndidzakupatsa luso loyimba mngoli, kusemasema ndi kujambula. Mwini wa zopangapanga zonse udzakhala iwe.
Ching’aning’ani:
Ukanditchula ine, udzakwatira mkazi amene ali wokongola mwa atsikana onse a ana a anthu.
[04.08]
Pamenepo mwana wa mnyamata adavutika ndi maganizo. Zimenezi sizinali zakutulo koma zoonadi. Mphamvu adali nazo, koma mpang’ono; ana anzake adamukanika kale, lero adali ndi mwayi wopeza mphamvu zowonjezera zomenyera! Ndiponso tsopano ndi akuluakulu omwe sadzamuopsanso. Kwinaku adasirira zoyimba ndi zopangapanga. Iye mwana wa mfumu akadatha kuvinitsa ndi akambuku omwe tsopano ndi nyimbo zake zotsekemera. Atate ake, akadawapangira mipando, matebulo, ndi mabedi omwe. Litsipa mbiri yake ikadamveka ponse.
[04.09]
Koma ganizo la mtsikana wokongola koposa azimayi ndi atsikana onse apansi pano lidamkondweretsa kwambiri. Sadatayenso nthawi posankha, adaweremira Ching’aning’ani. Namutchula mfumu ya anthu okongola onse. Azimu nthawi yomweyo sadachedwenso, Ching’aning’ani yekha adatsalira namfotokozera bwino za mtsikanayo. Dzina lake Namadanitsa. Adali kukhala ku dziko la Angitau ndi Ndaziona, mng’ono wake wa Zimeze.
[05.01]
Zinthu zonse zimayenda monga momwe adazipangira. Zonse zimayamba ndi kutha. Munthu akababwa amangochita zomwe adamulembera, kaya ndi tsoka kaya ndi mwayi, zonsezo amangokumana nazo, azifune kaya asazifune, mmomwemo. Namadanitsa ali ku madzi kukachapa ndi anamwali ake, adaona chinthu choyenda pamadzi chikubwera. Pochiyang’anitsitsa adaona kuti ndi ngalawa yaikulu. Atayang’anitsitsabe adaona kuti mudali anyamata ndi anthu akuluakulu.
[05.02]
Ngalawa itakocheza pa gombe, mkulu wa onse adatuluka ndi za nkhondo, nafunsa ngati atsikanawo adali kudziwa kumene kunali kukhala mfumu ina, Ndaziona, mphwake wa Zimeze, mfumu ya Angitau. Pamenepo Namadanitsa adadzuka ndikuyamba kumulonjera mlendoyo ndi anzake ena onse. Kenaka adafotokoza kuti, Ndaziona adali kukhala kumtunda kwenikweni kwa Nile, pafupi ndi Nyanja; Zimeze mkulu wake anali kukhala cham’munsi mwake. Namadanitsa adapitiriza kufotokoza kuti, ‘Pamene mwaimapo ndi pafupifupi ndi nyumba ya mfumu, imene simungaione chifukwa yabisika ndi mitengoyi. Mukafuna kukaona mfumuyo, ine mkazi wake, Namadanitsa ndikuperekezani ngati palibe choletsa.’
[05.03]
Pomvadzina la Namadanitsa, Litsipa adathunthumira ndi chimwemwe, nanyivula pang’ono nati: ‘Poti ndaona kumeneko kukhala ngati nkopitika ndi ngalawayi, talowani mom’muno ndi alezi anuwa, kuti tifulumire, chifukwa tikufuna tiyende mwamsanga.’ Mwamsangamsanga adanong’oneza mmalinyero wamkulu kuti asapitenso kunyumba kwawo.
[05.04]
Chosadziwa, mtsikana mmodzi sadalowe nawo adangobisala. Poona kuti ngalawa ikuthamanga pamadzi ulendo wa kwawo, mtsikana uja adakuwa ndi kulira mokweza ngati lipenga. Anthu adabwera kudzaona, koma adapeza Litsipa atapita kale, ali pafupinso kufika kwawo, Agangire poyendetsa ngalawa adali opambana.
[05.05]
‘Amayi, a Namadanitsa, abedwa ndi Agangire!’ adatero pouza anthu onse.
[05.06]
Ndaziona atamva zimenezo, zidamzula moyo! Sadathe kulira kapena kuyankhula. Atapeza nzeru, adasonkhanitsa anthu ake, nawafotokozera kuti mwa zolengedwa zonse, iye, Ndaziona, adalibe mnzake. Kameneka kadali kachiwiri kupeza milandu yotere, sabata yatha mwana wake wachisamba adampeza mikango itaphangirana. Kodi zimenezi zidali zotani?
[05.07]
Adatuma anthu asanu pa hatchi kukauza mkulu wake Zimeze, ndi kumdziwitsa kuti Gangire wamema nkhondo ya Angitau pomubera mkazi wake Namadanitsa. Iye yemwe adauza amisiri okonza ngalawa kuti akonzeke, adauzanso mulumuzana wake wa nkhondo kuti asonkhanitse anyamata amagazi ndi kuwapatsa zida za nkhondo. Mkulu wakenso atamva adachita chimodzimodzi. Posakhalitsa adatulukira ndi ngalawa zake za nkhondo.
[05.08]
Gangire wamkulu atamva zimene mwana wake adachitira Zimeze, pomubera mlamu wake, adadziwiratu kuti nkhondo ikubwera, adauza Kazione, mkulu wa nkhondo kuti akonzeke, chifukwa padalibenso chibwana.
[05.09]
Tsiku loti mawa ndi nkhondo anthu amaso, adaona kumwamba mbalame zikuluzikulu zikumenyana ndi kusosolana nthenga. Mbamba adayimba malipenga ake ndi kumenya ng’oma zake ‘Gulugulu!’ Sachokeka adadzadza ndi mabingu ndi zing’aning’ani. Kudziko la Agangire kudali bwalo lobulika bwino, lomwe pamachitikira masewera a mitundumitundu. Kalekale makolo omwe adaponyerapo nkhondo adafika ndi kudzadza.
[05.10]
Ku Ntheradi, Tinjiwa ndi anthu ake adagawikana, ena adafuna kuthandiza Angitau ena Agangire. Mitima ya anthu onse idagunda mopitiriza, nthumanzi idagwira aliyense.
[05.11]
Bwampini, Kazembe wamkulu wa Angitau onse ali pa hatchi, adatsogolera ankhondo onse a Angitau. Kazione naye adachita chimodzimodzi.
[05.12]
Maliro, zilonda, kulira, njala, nkhawa zidazadza ponseponse pa dziko la Sachokeka. Phokoso la mikondo, zibonga, mauta ndi nyankhwa zidagonthetsa makutu a anthu. Pherera, Kazembe wachiwiri wa Chingitau adasakaza Agangire kwabasi. Kumangowapha ngati adzowe. Iye chibadwire chake, mpeni, mkondo, muvi sizidathe kulowa m’chikopa chake. Chifukwa cha ichi adangopita dala pakati pa amaliwongo, omwe amamponyera mipeni, mikondo, mivi, koma osabaidwa. Naye Kazione, amene adali mwana wa Ching’aning’ani, chifukwa atate ake, Chokhola, amene adagona ndi Mzimuwu tsiku lina, ngakhale adali mkazi wamwini, nayenso adasakaza Angitau.
[05.13]
Utwa, mwana wamng’ono wa Gangire, nayenso adapambana koopsa. Munthu wamtali, wathupi, wodziwa kulewa ndi kuponya, adachitadi zachimuna.
[05.14]
Mitembo ya anthu akufa pambali zonse idakanika kukwiriridwa. Afisi ndi nyama zankhuli zonse zidachitadi chaka, mbalame zolusa monga ngwangwa, zidapeza chajira. Zimeze adavutika m’moyo poona mwana wa mchemwali wake Saopa, atabaidwa m’mimba ndi mkondo wa Kazione. Adaponya mivi ingapo kuti alase mdaniyo koma mivi inkangodya dothi; ina idalasa Agangire ena. Saopa adafa adakali mbeta yachimuna (akadali m’bwalo).
[05.15]
Pherera atalusa kwambiri, adathamanga pakati pa Agangire. Poona maponyedwe ake, osaphonya ndi osapherereka, ankhondo adamwazika. Poona zimenezo, Utwa adadzipereka nafuna kumenyana mikondo yokhayokha iye ndi Pherera. Pamenepo pakadakhala ngozi! Pherera, amene chida chilichonse sankaopsedwa nacho, adamgudukira mnzakeyo ndi kumponyera mkondo. Nthawi yomweyo padagwa mdima, mkondowo udamenya chikopa cha Ching’aning’ani amene adafuna kupulumutsa Utwa. Chifukwa cha mphamvu za Pherera, mkondowo udakalowa m’matumbo nutulukira. Komabe Utwa adagwa ndi mpemera, osabayidwa chifukwa cha Ching’aning’ani. Malipenga adalira, chifukwa kudali kutada. Anthu onse ankhondo adapita kuzithando zawo. Nthawi ya usiku adapeza nthawi yoyikira maliro ndi kupereka nsembe kwa akufa. Kutacha, mitima idada nkhawa bi.
[05.16]
Ankhondo adakumananso, ‘Kho! Kho! Thwe! Thwe! Mayo!’ Phokoso lidamvekanso ponseponse. Bwampini ndi nzeru zake zopambana adaonetsa kukula kwa umisiri wake wa nkhondo. Atapangana ndi Pherera, kubwalo la nkhondo kudapita anthu ochepa Achingitau. Pompo Utwa ndi Kazione adapusitsidwa, naganiza kuti Angitau kugonja kwawo kudali tsikulo, osatinso lina.
[05.17]
Koma iwowo sadamudziwe Bwampini. Iye adapanga chihatchi chake chosema, chachikulu. Ankhondo ambiri adalowa mmenemo, ulendo wa Zimeze, Ndaziona, Chamuna ndi ankhondo ena onse otchuka. Ankhondo ena adachiyendetsa chihatchi chija pakati pa usiku mpaka pafupi ndi chipata chamzinda waukulu wa Gangire – Huwa. Podzuka Agangire adapeza chihatchi chokongola, chosema, nazizwa nacho kwambiri. Akazi, ana, nkhalamba ndi amuna onse odwala amene adakhala kunkhondo adachiyang’anitsitsa kwabasi ndi kuchita nacho chidwi. Adachikankha nachilowetsa mumzinda wawo. Naganiza kuti mwina iyi ndi mphatso yachipepeso yochokera kwa Angitau.
[05.18]
Namadanitsa nayenso adabwera, nachiyang’anitsitsa. Atachiona iye adauza Agangire kuti mudali anthu m’katimo, koma adamutsutsa, namseka. Iye adayesetsa kuyankhula zambiri zofuna kuseketsa am’katimo koma adalephera. Agangire atachiyang’anitsitsa chinthu chachilendocho ndi kutopa nacho, adachoka ndi kupita kwawo.
[05.19]
Usiku, anthu onse atachoka nakagona, Bwampini adauza ankhondo aja kuti atuluke. Onse adataluka ndikumenya nkhondo yakabisalira mpaka kutsegula zipata za mzinda. Ankhondo ena a Chingitau adalowa natentha Huwa, nagwira mfumu Gangire; napha amuna onse mumzinda ndi nkhalamba zomwe, koma atsikana ndi tchembere zachitsikana zidatengedwa. Utwa ndi Kazione adadodoma ndi umambala wa Bwampini, adangodzipereka, ndipo nkhondo idathera pompo. Awiriwa sadaphedwe.
[05.20]
Zimeze, atatenga chuma cha Huwa ndi atsikana omwe, adalamula ankhondo ake kuti asonkhane. Adachita chaka choti agonjetsa Gangire, napereka nsembe zothokoza Azimu, makamaka Mziisi [Ndomondo], amene adathandizadi kopambana kulira akufa. Kenaka adalamula ulendo wobwerera ku nyumba. Anthu obwerera kunyumba adali ochepa. Mwa ngalawa makumi asanu zomwe zidabwerera, makumi atatu adadzaza ndi anthu amoyo, chuma cha Huwa ndi atsikana Achigangire.